Blackafella New Song Amangolira tackles Ufulu wa Achinyamata
by GhettoTunes
Pamene dziko la Malawi likukondwelera kukwanisa zaka 59, Blackafella wakambapo za mmene Achinyamata komaso anthu ena akukhalira mmuno ma Malawi.
Oyimba wa gulu la Don Dadaz yu wadandaula momwe akulu akulu akuyendesera zinthu dziko muno kupangisa moyo wachinyamata kukhala olimba pano pa Malawi.
Blackafella Man ah Complex anenapo kuti, "Mvula ikagwa mafana amangoliralira, Palibe chomwe boma likuwachitira".
Izi zikutanthauza kuti feteleza amavuta kupeza pamene nyengo yolima yafika. Koma iye wanenapo kuti ngakhale zimachitika chonchi Ghetto Yut ndi Star ali ndi kuthekera kopanga zinthu zopitisa dziko li patsogolo atapasidwa mwayi ndi zoyeneleka zose.
Nyimbo yagwilidwa mwa ukadaulo ndi ma producer awili M.O.D mophatikizana ndi Warge Records.
Iye Walangizaposo kuti ingokhalani phe osazipopa, zosezi nza namalenga Jah. Ghetto Yut usatuluse mfuti, kutchola nyumba, Kufwamba Njeee.
"Komwe muliko Muziuzana, Ah Jokes nthabwala zanuzo muziuza Ana, Chomwe Chachuluka pa Malawi mchibwana, Palibe Kufooka lero tithana tithana, Osamapusisana".
Stream/Download Amangolira on the link http://ghettotunes.com/stream?a=76458
.
.
Up Next
Go mobile
© Copyright 2023